Webusaiti Yovomerezeka ya Mboni za Yehova

Pa chiyambi Beliefs Future Medical Topics Titumizireni Adiresi Yanu Publications Languages
Baibulo

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Kodi Zikuchitikazi Ndi Cholinga cha Mulungu?


MITU

  1. Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
  2. Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
  3. Kodi Mulungu Ali Nalo Cholinga Chotani Dziko Lapansili?
  4. Kodi Yesu Kristu Ndani?
  5. Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse
  6. Kodi Akufa Ali Kuti?
  7. Chiyembekezo Chotsimikizika Chokhudza Okondedwa Anu Amene Anamwalira
  8. Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  9. Kodi Tili ‘M’masiku Otsiriza’?
  10. Mmene Zolengedwa Zauzimu Zimakhudzira Moyo Wathu
  11. N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
  12. Kukhala ndi Moyo Wokondweretsa Mulungu
  13. Onani Moyo Mmene Mulungu Amauonera
  14. Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Likhale ndi Moyo Wosangalala
  15. Kupembedza Kumene Mulungu Amavomereza
  16. Imani Zolimba ku Mbali ya Kupembedza Koona
  17. Yandikirani kwa Mulungu M’pemphero
  18. Ubatizo ndi Ubale Wanu ndi Mulungu
  19. Khalanibe M’chikondi cha Mulungu

Pulintani tsamba ili Pulintani tsamba ili

WERENGANI nyuzipepala ina iliyonse. Onererani TV, kapena mvetserani wailesi. Pali nkhani zambirimbiri za upandu, nkhondo, ndi uchigawenga. Ndiyeno ganizirani mavuto anu. Mwinamwake ndinu wachisoni kwambiri chifukwa chakuti munthu amene mumam’konda akudwala kapena anamwalira. Mungamamve ngati mmene munthu wabwino Yobu anamvera. Yobu ananena kuti “ndakhuta mavuto.”—Yobu 10:15, The Holy Bible in the Language of Today.

Dzifunseni kuti:

Baibulo lili ndi mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa.

BAIBULO LIMAPHUNZITSA KUTI MULUNGU ADZACHITA ZOTSATIRAZI PA DZIKO LAPANSI.

Munthu wachikulire wakhalanso mnyamata

“Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.”—Chivumbulutso 21:4


Mtsikana wolumala akuthanso kuthamanga

“Wopunduka adzatumpha ngati nswala.”—Yesaya 35:6


Munthu wosaona wayambiranso kuona

“Maso a akhungu adzatsegudwa.”—Yesaya 35:5


Mayi wasangalala ataona wokondedwa wake atauka kwa akufa

“Onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29, NW


Mnyamata amene anali kudwala akuchira

“Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24


Minda ya chakudya

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.”—Salmo 72:16


PINDULANI NDI ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA

Anthu awiri akuphunzira Baibulo

Musafulumire kuganiza kuti zimene zanenedwa ndi maganizo chabe okhumba zinthu zabwino. Mulungu walonjeza kuti adzachita zimenezi, ndipo Baibulo limalongosola mmene adzazichitira.

Koma Baibulo limathandizanso pambali zina. Limafotokoza chinsinsi cha mmene mungakhalire ndi moyo wosangalatsadi ngakhale panopo. Taganizirani kaye zinthu zimene zimakudetsani nkhawa komanso mavuto amene muli nawo. Zimenezi zingakhudze kusowa ndalama, mavuto a banja, kudwala, kapena kumwalira kwa munthu amene mumam’konda. Baibulo lingakuthandizeni kuthana ndi mavuto masiku ano, ndipo lingakutsitsimuleni mwa kuyankha mafunso onga ngati awa:

Kuwerenga buku lino kumene mukuchitaku ndi umboni wakuti mukufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Buku lino likuthandizani. Onani kuti ndime iliyonse ili ndi funso lake m’munsi mwa tsamba limenelo. Anthu ambiri aikonda njira yogwiritsa ntchito mafunso ndi mayankho pokambirana za m’Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tikukhulupirira kuti inunso muikonda. Mulungu akudalitseni pamene tsopano mukuyamba kuona kusangalatsa kwake kwa kuphunzira zimene Baibulo kwenikweni limaphunzitsa!

LIDZIWENI BWINO BAIBULO LANU

Baibulo

M’Baibulo muli mabuku ndi makalata ndipo onse pamodzi amakwana 66. Mabuku ndi makalata amenewa anawagawa m’machaputala ndi mavesi kuti asamavute kupeza. Tikamatchula malemba m’buku lino, nambala yoyambirira kuchokera pa dzina la buku kapena kalata ya m’Baibuloyo ikuimira chaputala, pamene nambala yotsatira yakeyo ikuimira vesi. Mwachitsanzo, tikalemba kuti “2 Timoteo 3:16” zikutanthauza kuti kalata yachiwiri yopita kwa Timoteo, chaputala 3, vesi 16.

Simuchedwa kulizolowera Baibulo ngati muziwerenga m’Baibulolo malemba amene asonyezedwa m’buku lino. Ndiponso, bwanji osakonza pulogalamu yakuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse? Mutati muziwerenga machaputala atatu mpaka asanu pa tsiku, mukhoza kuwerenga Baibulo lonse pakutha chaka.

PamwambaPatsogolo

Lofalitsidwa mu 2005